Deuteronomo 4:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe.

5. Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzicita cotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu Lanu.

6. Cifukwa cace asungeni, aciteni; pakuti ici ndi nzeru zanu ndi cidziwitso canu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukuru uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.

7. Pakuti dioloketu mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene pali ponse timaitanira iye?

Deuteronomo 4