11. Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phizilo linayaka mota kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.
12. Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.
13. Pamenepo anakufotokozerani cipangano cace, cimene anakulamulirani kucicita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.
14. Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawacite m'dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanu lanu.
15. Potero dzicenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenya mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu m'Horebe, ali pakati pa moto;
16. kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga cifaniziro ciri conse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;
17. mafanidwe a nyama iri yonse iri pa dziko lapansi, mafanidwe a mbalame iri yonse yamapiko yakuuluka m'mlengalenga,
18. mafanidwe a cinthu ciri conse cokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iri yonse yokhala m'madzi pansi pa dziko;