Deuteronomo 32:34-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Kodi sicisungika ndi Ine,Colembedwa cizindikilo mwa cuma canga ceni ceni?

35. Kubwezera cilango nkwanga, kubwezera komwe,Pa nyengo ya kuterereka phazi lao;Pakuti tsiku la tsoka lao layandika,Ndi zinthu zowakonzeratu zifulomira kudza.

36. Popeza Yehova adzaweruza anthuace,Nadzacitira nsoni anthu ace;Pakuona iye kuti mphamvu yao yatha,Wosatsala womangika kapena waufulu,

37. Pamenepo adzati, Iri kuti milunguyao,Thanthwe limene anathawirako?

38. Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera,Nimwa vinyo wa nsembe yao yothira?Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.

39. Tapenyani tsopano kuti Ine ndine iye,Ndipo palibe mulungu koma Ine;Ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi mayo:Ndikantha, ndicizanso Ine;Ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.

40. Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba,Ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,

41. Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Ndi dzanja langa likagwira ciweruzo;Ndidzabwezera cilango ondiukira,Ndi kulanga ondida.

42. Mibvi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,Ndi lupanga langa lidzalusira nyama;Ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,Ndi mutu wacitsitsi wa mdani,

43. Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ace;Adzalipsira mwazi wa atumiki ace,Adzabwezera cilango akumuukira,Nadzafafanizira zoipa dziko lace, ndi anthu ace.

Deuteronomo 32