9. Nkhondo yanu ikaturuka pa adani anu, mudzisunge kusacita coipa ciri conse.
10. Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera cifukwa cocitika usiku, azituruka kunja kwa cigono, asalowe pakati pa cigono;
11. koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa cigono.
12. Mukhale nao malo kunja kwa cigono kumene muzimukako kuthengo;
13. nimukhale naco cokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe naco, ndi kutembenuka ndi kufotsera cakuturukaco;