Deuteronomo 23:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Munthu wophwetekwa, wophwanyika kapena wofulika, asalowe m'msonkhano wa Yehova.

2. Mwana wa m'cigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wace wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.

3. M-amoni kapena Mmoabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;

4. popeza sanakukumikani ndi mkate ndi madzi m'njira muja munaturuka m'Aigupto; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesapotamiya, kuti akutemberereni.

5. Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafuna kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.

Deuteronomo 23