8. Potero tinapitirira abale athu, ana a Bsau okhala m'Seiri, njira ya cidikha, ku Elati ndi ku Ezioni Geberi.
9. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya cipululu ca Moabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usabvuta Moabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lace likhale lako lako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale lao lao.
10. (Aemi anakhalamo kale, ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, ngati Aanaki.
11. Anawayesa iwonso Arefai, monga Aanaki; koma Amoabu awacha Aemi.
12. Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israyeli anacitira dziko lace lace, limene Yehova anampatsa.)