10. Ndipo mucite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kucita monga mwa zonse akulangizanizi,
11. Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa ciweruzo akufotokozerani, mucite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.
12. Koma munthu wakucita modzikuza, osamvera wansembe wokhala ciriri kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo mucotse coipaco kwa Israyeli.
13. Ndipo anthu onse adzamva ndi kucita mantha, osacitanso modzikuza.
14. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanu lanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;