1. Pakutha Pace pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale cilekerero.
2. Cilekereroco ndici: okongoletsa onse alekerere cokongoletsa mnansi wace; asacifunse kwa mnansi wace, kapena mbale wace; popeza analalikira cilekerero ca Yehova.
3. Muyenera kucifunsa kwa mlendo; koma canu ciri conse ciri ndi mbale wanu, dzanja lanu licilekerere;
4. ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu;
5. cokhaci mumvere cimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kucita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.
6. Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monza ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzacita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzacita ufumu pa inu.