29. Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamacita mantha nao.
30. Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakucitirani m'Aigupto pamaso panu;
31. ndi kucipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wace wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.
32. Koma m'cinthu ici simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu,
33. amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi mota usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.
34. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,
35. Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.