8. Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukuru, koma atakhala wamphamvu, nyanga yace yaikuru inatyoka; ndi m'malo mwace munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza ku mphepo zinai za mlengalenga.
9. Ndipo mu imodzi ra izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukuru ndithu, kuloza kumwela, ndi kum'mawa, ndi ku dziko lokometsetsa.
10. Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza.
11. Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimcotsera nsembe yopsereza yacikhalire; ndi pokhala malo ace opatulika panagwetsedwa.