13. Pamenepo ndinamva wina woyera, alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yacikhalire, ndi colakwa cakupululutsa ca kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?
14. Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.
15. Ndipo kunali, nditaona masomphenyawo, ine Danieli ndinafuna kuwazindikira; ndipo taonani, panaima popenyana ndi ine ngati maonekedwe a munthu.
16. Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabrieli, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.