Danieli 5:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. popeza m'Danieli yemweyo, amene mfumu adamucha Belitsazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi cidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa, ndi kumasula mfundo. Amuitane Danieli tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.

13. Pamenepo analowa naye Danieli kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, Ndiwe kodi Danieli uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?

14. Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.

Danieli 5