Danieli 4:34-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumcitira ulemu Iye wokhala cikhalire; pakuti kulamulira kwace ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wace ku mibadwo mibadwo;

35. ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa acabe; ndipo Iye acita mwa cifunito cace m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lace, kapena wakunena naye, Mucitanji?

36. Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi cifumu canga ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akuru anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandioniezeranso ukulu wocuruka.

37. Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti nchito zace zonse nzoona, ndi njira zace ciweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwacepetsa.

Danieli 4