1. Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere ucurukire inu.
2. Candikomera kuonetsa zizindikilo ndi zozizwa, zimene anandicitira Mulungu Wam'mwambamwamba.
3. Ha! zizindikilo zace nzazikuru, ndi zozizwa zace nza mphamvu, ufumu wace ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwace ku mibadwo mibadwo.