1. Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolidi, msinkhu wace mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lace mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa cidikha ca Dura, m'dera la ku Babulo.
2. Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga cuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzurula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.
3. Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga cuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.