Danieli 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaeli kalonga wamkuru wakutumikira ana a anthu amtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi, yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.

2. Ndipo ambiri, a iwo ogona m'pfumbi lapansi adzauka, ena kumka ku moyo wosatha, ndi ena ku manyazi ndi mnyozo wosatha.

3. Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate cilungamo ngati nyenyezi ku nthawi za nthawi.

4. Koma iwe Danieli, tsekera mau awa, nukomere cizindikilo buku, mpaka nthawi ya cimariziro; ambiri adzathamanga cauko ndi cauko, ndi cidziwitso cidzacuruka.

Danieli 12