2. Ndipo tsopano ndikufotokozera coonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Perisiya, ndi yacinai idzakhala yoletnera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwace idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Helene.
3. Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzacita ufumu ndi ulamuliro waukuru, nidzacita monga mwa cifuniro cace.
4. Ndipo pakuuka iye ufumu wace udzatyoledwa, nudzagawikira ku mphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yace akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wace anacita ufumu nao; pakuti ufumu wace udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.