1. Ndipo ine, caka coyamba ca Dariyo Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.
2. Ndipo tsopano ndikufotokozera coonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Perisiya, ndi yacinai idzakhala yoletnera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwace idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Helene.
3. Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzacita ufumu ndi ulamuliro waukuru, nidzacita monga mwa cifuniro cace.