10. Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.
11. Nati kwa ine, Danieli, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndirikunena ndi iwe, nukhale ciriri; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.
12. Pamenepo anati kwa ine, Usaope Danieli; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzicepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako,
13. Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.
14. Ndadzera tsono kukuzindikiritsa codzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.
15. Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala du.
16. Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, cifukwa ca masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndiribenso mphamvu.