Danieli 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. CAKA cacitatu ca Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo.

2. Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lace, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye ku dziko la Sinara, ku nyumba ya mulungu wace, nalonga zipangizozo m'nyumba ya cuma ca mulungu wace.

3. Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkuru wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israyeli, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga;

4. anyamata opanda cirema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ocenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'cinyumba ca mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Akasidi.

5. Ndipo mfumu inawaikira gawo la cakudya ca mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pace aimirire pamaso pa mfumu.

6. Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Danieli, Hananiya, Misayeli, ndi Azariya.

7. Ndi mkuru wa adindo anawapatsa maina ena; Danieli anamucha Belitsazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaeli, Mesaki; ndi Azariya, Abedinego.

8. Koma Danieli anatsimikiza mtimti kuti asadzidetse ndi cakudya ca mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; cifukwa cace anapempha mkuru wa adindo amlole asadzidetse.

9. Ndipo Mulungu anamkometsera Danieli mtima wa mkuru wa adindo, amcitire cifundo.

Danieli 1