Cibvumbulutso 8:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi ciwiri, munali cete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

2. Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.

Cibvumbulutso 8