Cibvumbulutso 7:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Cifukwa cace ali ku mpando wacifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira iye usana ndi usiku m'Kacisi mwace; ndipo iye wakukhala pa mpando wacifumu adzawacitira mthunzi,

16. sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena, silidzawatentha dzuwa, kapena citungu ciri conse;

17. cifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wacifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.

Cibvumbulutso 7