12. akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira cilimbiko, ndi cuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ciyamiko.
13. Ndipo colengedwa ciri conse ciri m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva zirikunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale ciyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthawi za nthawi.
14. Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuruwo anagwa pansi nalambira.