Cibvumbulutso 5:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la iye wakukhala pa mpando wacifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwace, losindikizika ndi zizindikilo zisanu ndi ziwiri.

2. Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau akuru, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikilo zace?

3. Ndipo sanathe mmodzi m'Mwamba, kapena padziko, kapena pansi pa dziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.

4. Ndipo ndinalira kwambiri, cifukwa sanapezedwa mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;

5. ndipo mmodzi wa akuru ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wocokera m'pfuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikilo zace zisanu ndi ziwiri.

Cibvumbulutso 5