Cibvumbulutso 3:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndidziwa nchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

16. Kotero, popeza uti wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m'kamwa mwanga.

17. Cifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo cuma ndiri naco, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wocititsa cifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

Cibvumbulutso 3