1. Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidaeoka, ndipo kulibenso nyanja.
2. Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wace.
3. Ndipo ndinamva mau akuru ocokera ku mpando wacifumu, ndi kunena Taonani, cihema ca Mulungu ciri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ace, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;