Cibvumbulutso 17:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa cifukwa ninji? ine ndidzakuuza iwe cinsinsi ca mkazi, ndi ca cirombo cakumbereka iye, cokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

8. Cirombo cimene unaciona cinaliko, koma kulibe; ndipo cidzaturuka m'phompho, ndi kunka kucitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo ciyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona cirombo, kuti cinaliko, ndipo kulibe, ndipo cidzakhalako.

9. Pano pali mtima wakukhaia nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;

10. ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iriko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi.

Cibvumbulutso 17