Cibvumbulutso 13:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaimirira pa mcenga wa nyanja.Ndipo ndinaona cirombo cirinkuturuka m'nyanja, cakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ow iwiri, ndi pa nyanga zace nduwira zacifumu khumi, ndi pamitu pace maina a mwano.

2. Ndipo cirombo ndinacionaco cinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ace ngati mapazi a fisi, ndi pakamwa pace ngati pakamwa pa mkango; ndipo cinjoka cinampatsa iye mphamvu yace, ndi mpando wacifumu wace, ndi ulamuliro waukuru.

Cibvumbulutso 13