Cibvumbulutso 12:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.

12. Cifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.

13. Ndipo pamene cinjoka cinaonakuticinaponyedwa pansikudziko, cinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.

14. Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a ciombankhanga cacikuru, kuti akaulukire kucipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.

15. Ndipo inalabvulira m'kamwa mwace, potsata mkazi, madzi ngati mtsinje, kuti akakokoleredwe mkazi nao.

Cibvumbulutso 12