21. Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.
22. Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro cace moyo wosatha.
23. Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.