Aroma 3:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ciani tsono? kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi ucimo;

10. monga kwalembedwa,Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;

11. Palibe mmodzi wakudziwitsa, Palibe mmodzi wakuloodola Mulungu;

12. Onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pace;Palibe mmodzi wakucita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.

13. M'mero mwao muli manda apululu;Ndi lilime lao amanyenga; Ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;

14. M'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;

15. Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;

Aroma 3