6. Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanieniemera anthu? Kodi coipa cidzagwera mudzi osacicita Yehova?
7. Pakuti Ambuye Yehova sadzacita kanthu osaulula cinsinsi cace kwa atumiki ace aneneri.
8. Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?
9. Bukitsani ku nyumba zacifumu za Asidodi, ndi ku nyumba zacifumu za m'dziko la Aigupto, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akuru m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwace.
10. Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.