5. Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.
6. Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa iye,
7. ozika mizu ndi omangirika mwa iye, ndi okhazikika m'cikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kucurukitsa ciiyamiko.
8. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati cuma, mwa kukonda nzeru kwace, ndi cinyengo copanda pace, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu;