Akolose 2:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo cifukwa ca inu, ndi iwowa a m'Laodikaya, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;

2. kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'cikondi, kufikira cuma conse ca cidzalo ca cidziwitso, kuti akazindikire Iwo cinsinsi ca Mulungu, ndiye Kristu,

3. amene zolemera zonseza nzeru ndi cidziwitso zibisika mwa iye.

4. Ici ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.

5. Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.

Akolose 2