24. Tsopano 1 ndikondwera nazo zowawazo cifukwa ca inu, ndipo 2 ndikwaniritsa zoperewera za cisautso ca Kristu m'thupi langa 3 cifukwa ca thupi lace, ndilo Eklesiayo;
25. amene ndinakhala mtumiki wace, 4 monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakucitira inti, wakukwaniritsa mau a Mulungu,
26. 5 ndiwo cinsinsico cinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anacionetsa tsopano kwa oyera mtima ace,
27. kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ici 6 cimene ciri cuma ca ulemerero wa cinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Kristu mwa inu, ciyembekezo ca ulemerero;
28. amene timlalikira ife, ndi kucenjeza munthu ali yense 7 ndi kuphunzitsa munthu ali yense mu nzeru zonse, 8 kuti tionetsere munthu ali yense wamphumphu mwa Kristu;
29. kucita ici ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa 9 monga mwa macitidwe ace akucita mwa ine ndi mphamvu.