17. Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.
18. Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba.
19. Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire,
20. mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.
21. Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'cifuwa canu m'nchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani