Ahebri 9:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo cingakhale cipangano coyambaci cinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.

2. Pakuti cihema cidakonzeka, coyamba cija, m'menemo munali coikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika,

Ahebri 9