Agalatiya 1:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. umene suli wina; koma pali ena akubvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Kristu.

8. Koma ngakhale ife, kapena mngelo wocokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.

9. Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.

10. Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Kristu.

11. Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

12. Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu Kristu.

13. Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Ciyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

14. ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Ciyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wacangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

15. Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa cisomo cace,

Agalatiya 1