9. ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;
10. kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu ya kuuka kwace, ndi ciyanjano ca zowawa zace, pofanizidwa ndi imfa yace;
11. ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.
12. Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.
13. Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,
14. ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.
15. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;