Aefeso 4:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. ngatitu mudamva iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa iye, monga coonadi ciri mwa Yesu;

22. kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;

23. koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

24. 2 nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca coonadi.

25. Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.

26. 5 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe muli cikwiyire,

27. ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.

Aefeso 4