2 Timoteo 3:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. osayera mtima, opanda cikondi cacibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,

4. aciwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;

5. akukhala nao maonekedwe a cipembedzo, koma mphamvu yace adaikana; kwa iwonso udzipatule,

6. Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundu mitundu:

7. ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira ku cizindikiritso ca coonadi.

8. Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana naco coonadi; ndiwo anthu obvunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pacikhulupiriro.

2 Timoteo 3