11. Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzacita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
12. Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lace ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.
13. Comweco Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ace onse awiri.