2 Samueli 7:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cifukwa cace tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakucotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israyeli,

9. Ndipo ndinali nawe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akuru ali pa dziko lapansi,

10. Ndipo ndidzaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawabvutanso, monga poyamba paja,

11. monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

2 Samueli 7