7. Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, cifukwa ca kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.
8. Ndipo kudaipira Davide, cifukwa Yehova anacita cipasulo ndi Uza; nacha-malowo Cipasulo ca Uza, kufikira lero lino.
9. Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?
10. Momwemo Davide sanafuna kudzitengera likasa la Yehova lidze ku mudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.