2 Samueli 5:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Cinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mudzi wa Davide.

8. Ndipo tsiku lija Davide anati, Ali yense akakantha Ajebusi, aponye m'madzi opuala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Cifukwa cace akuti, Akhungu ndi opuala sangalowe m'nyumbamo.

9. Ndipo Davide anakhala m'linga mula, nalicha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.

10. Ndipo Davide anakula cikulire cifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.

2 Samueli 5