2 Samueli 19:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kucita comkomera. Ndipo Simeyi mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordano.

19. Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukile cimene mnyamata wanu ndinacita mwamphulupulu tsiku lila mbuye wanga mfumu anaturuka ku Yerusalemu, ngakhale kucisunga mumtima mfumu.

20. Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.

21. Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simeyi cifukwa ca kutemberera wodzozedwa wa Yehova?

2 Samueli 19