13. Ndiponso ngati walowa ku mudzi wina, Aisrayeli onse adzabwera ndi zingwe kumudziko, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko.
14. Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israyeli anati, Uphungu wa Husai M-ariki uposa uphungu wa Ahitofeli. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofeli kuti Yehova akamtengere Abisalomucoipa.
15. Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abyatara ansembewo, Ahitofeli anapangira Abisalomu ndi akuru a Israyeli zakuti zakuti; koma ine ndinapangira zakuti zakuti.
16. Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.