20. Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofeli, Upangire cimene ukuti rikacite.
21. Ndipo Ahitofeli ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi ang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisrayeli onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.
22. Comweco iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi ang'ono a atate wace pamaso pa Aisrayeli onse.
23. Ndipo uphungu wa Ahitofeli anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofeli unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.