2 Petro 3:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwace kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha mota idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuru.

13. Koma monga mwa lonjezano lace tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi ziko latsopano m'menemo mukhalitsa cilungamo.

14. Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.

15. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;

16. monganso m'akalata ace onse pokanba momwemo za izi; m'menemo nuli zina zobvuta kuzizindikira, zinene anthu osaphunzira ndi osachazikika apotoza, monganso atero lao malembo ena, ndi kudziononga lao eni.

2 Petro 3