3. Naikanso gawo la mfumu lotapa pa cuma cace la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova.
4. Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'cilamulo ca Yehova.
5. Ndipo pobuka mau aja, ana a Israyeli anapereka mocuruka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uci, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mocuruka.
6. Ndi ana a Israyeli ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyuru miyuru,